Mbiri ya martse Martin Nkhata
>> YOUR LINK HERE: ___ http://youtube.com/watch?v=rbc04X_ocos
if you like my content and would like to support me further, please • PayPal • ➡️To Donate please use PayPal https://www.paypal.me/hanifamalawi • Business/Sponsor Inquiries //[email protected] • MARTSE WAPITA • Pa 25 May mchaka cha 2022, mtundu wa a Malawi unakhamukira ku bwalo la Civo mu mzinda wa Lilongwe komwe kunali mwambo woperekeza ulendo womaliza wa woyimba waluso Martin Nkhata yemwe ambiri amaudziwa ndi dzina lakuti Martse. Martse anamwalira pa 23 May 2022 ku chipatala cha Queen Elizabeth Hospital (QECH) komwe amalandira thandizo la mankhwala atavulala pa ngozi ya moto yomwe inachitika ku Mangpchi komwe anali ku tchuthi. Imfa ya Martse yakhuza anthu ambiri mdziko muno popeza wamwalira ali wachichepere komanso sanadwale. Kuyambira anthu achikulire, achinyamata pamodzi ndi ana amadziwa Martse kudzera ku nyimbo zake zomwe wakhala akuyimba nthawi yomwe anali moyo monga Mwapindulanji, Mabala, Zikomo, Mwano, Dosage, Adidas ndi zina zambiri. Ngakhale anthu mdziko muno amayesa kuti nyimbo za chamba cha Hip Hop sizipita patali, koma ayi ndithu zonsezi zawonetsa kuti ndi bodza chabe malingana ndi mmene anthu anadzazira ku mwambo wamaliro ake ku bwalo la Civo. Martse amakondedwa, nyimbo zake zinali zokhuza aliyense, zachikondi monga Mwano ndi Dosage komanso zomenyera ufulu monga Mabala, Malume kungotchulapo zochepa. Anthu ali mu chisoni ndipo dziko zinthu zinayima kamba ka imfa yake
#############################
New on site